Kugwiritsa Ntchito Moyenera Masamba Amchezo

Feb 28, 2025Articles0 comments

Bungwe la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lapempha achinyamata kuti azigwiritsa ntchito moyenera masamba amchezo osati kunyoza kapena kubweretsa chisokonezo mdziko pomwe dziko lino lichititse chisankho posachedwapa Malinga ndi m’modzi wa oyendetsa ntchito ku CMD a Dalitso Magelegele, achinyamta ambiri akumagwiritsa ntchito maina ozimbayitsa ‘zigoba’ komanso masamba awo enieni kunyoza ena ponena kuti izi sizabwino pa ulamuliro wa demokalese.
“Tigwiritse ntchito masamba athu amchezo kukamba mfundo za omwe timawasapotera,” iwo atero.
Iwo ayankhula izi ku Mzuzu pa ulendo wa ndalawala omwe unakonzedwa ndi ofesi ya achinyamata ndi thandizo lochokera ku bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Public Trust.
Ndipo mkulu oyang’anila za apolisi a m’madera ku Mzuzu a Alexander Ngwala ati achinyamata ali ndi udindo olewa kugwiritsidwa ntchito poyambitsa ziwawa.
Wolemba Feston Malekezo
You may like also

0 Comments

Submit a Comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *

CMD